Yesu Bwenzi Mtimanga
[1]
Yesu, Bwenzi Mtimanga, Ndithawira kwanuko.
Pakuka madziwo, Pakuomba mphepoyo.
Mundibise Mbuyanga, Likaleka bvutolo,
Mnditsogoze bwinotu, Mndilandire kwanuko.
[2]
Pobisala panai, Ndingokangamira ’Nu.
Ndiri wosauka ’ne, Mbuye, msandiyedi.
Wondithandiza wanga ’Nu, Ndikukhulupira ’Nu,
Mu mapiko anuwo Mundipfunde inedi.
[3]
Kristu, Mukwaniradi, Mndikhutitse mmtimanga;
Msangalatse ifetu, Obvutika tonsefe.
Ine ndi woipadi! Inu wakuyera mbu;
Ine ndi wongengadi, Woonadi inutu.
[4]
Nsoni zanu ziinga Zakuipa zangazo
Mundisunge woti mbe, Ee! Ndi mwazi wanuwo.
Pa citsime canuco Mundimwetse Inudi;
Mtima wanga madziwo. Adzayendayendabe.
Support Mysongbooks
Support us by joining the Buy Me A Coffee community and making a small donation, you can help us expand our library and ensure that music lovers everywhere can enjoy their favorite songs to the fullest. We're passionate about music, and we know you are too, so let's work together to keep the music alive.
Thank you for being a part of our community and supporting our mission to provide the best lyrics library on the internet.