Uyang’ane Mdaniyo
[1]
Mkhristuwe dzuka! Alamula Mbuye;
Tenga cikopa, ndi lupanga m’dzanja,
Ukomane naye, usamuope
Ulimbe Mtima, Myang’ane mdaniyo.
Refrain:
Limba Mtima, Limba Mtima,
Limba Mtima, Pom’yang’ana mdani.
[2]
Zoopsa ziripo, ucenjeretu,
Usafulatire, ungapwekekwe;
Unyinji wa ’dani, udzagonjetsa,
Ulimbe Mtima, M’yang’ane mdaniyo.
[3]
Ntchito ya Mbuyako uiteteze;
Dzukatu mwa cangu nkhondoyo ithe;
Akakulamula, pita mwa cangu,
Ulimbe Mtima M’yang’ane mdaniyo.
[4]
Pita limbikira, suli wekhai,
Mwayi apatsa, cisangalatsonso;
Mwayi apatsa, cisangalatsonso;
Cikondi cace ngati mtsinje m’tengo;
Ulimbe Mtima M’yang’ane mdaniyo
Support Mysongbooks
Support us by joining the Buy Me A Coffee community and making a small donation, you can help us expand our library and ensure that music lovers everywhere can enjoy their favorite songs to the fullest. We're passionate about music, and we know you are too, so let's work together to keep the music alive.
Thank you for being a part of our community and supporting our mission to provide the best lyrics library on the internet.