Omba Lipenga
[1]
Mlonda lalika uthenga, Chenjeza anthu onse,
Iye wakumva adzetu, Nakhale nawo moyo.
Chorus:
Omba Lipenga mlonda’we, Anthu onse amvetu
Lalika atero Mlungu! Onse amasulidwe.
[2]
Lalika m’mapiri monse, Mnkhalango ndi m’madambo;
Lalikiranso mzinyanja, Ndi nyimbo yokondwera.
[3]
Lalikira ponse ponse, kumene kuli mdima;
Amve kuti zonse zapsa, Atate alindira.
[4]
Lalikira kwa otodwa, Akufuna mpumulo;
Yesu ali kuitana, Idzani kwa inetu.
Support Mysongbooks
Support us by joining the Buy Me A Coffee community and making a small donation, you can help us expand our library and ensure that music lovers everywhere can enjoy their favorite songs to the fullest. We're passionate about music, and we know you are too, so let's work together to keep the music alive.
Thank you for being a part of our community and supporting our mission to provide the best lyrics library on the internet.