Loading Songs...

Nkhoswe Yadza

[1]
Lalikira mau konse kuli anthu
A mtima wosowa A m’dziko latsoka,
Mkhristu ali yense Anene mokondwa
Nkhoswe yafikadid!

Chorus:
Nkhoswe yafikadi, Nkhoswe yafikadi!
Mzimu wa Mulungu pangano la Mbuye;
Lalikira mau Konse kuli anthu,
Nkhoswe yafikadi!

[2]
Usiku wapiti, Kunja nako kwaca;
Kulira kwaleka, Ndi mkwiyo naonse,
Pamapiri napo Dzuwa lioneka;
Nkhoswe yafikadi!

[3]
Mfumu ya mafumu ibwera ndi mwayi,
Kwa ocimwa onse Kudzapulumutsa;
M’malomo mwa cete Mumveka nyimbo
Nkhoswe yafikadi!

[4]
Cikondi cakuya Ndicimene bwanji,
Kwa anthu ocimwa Apeze cisomo, Wocimwa ngati’ne Ndingawale bwanji;
Nkhoswe yafikadi!

[5]
Kuyimba kumveke Mlengalenga monse;
Oyera a m’mwamba Ndi a pansi pano
Abvomerezane Nyimbo yacikondi,
Nkhoswe yafikadi!



Support Mysongbooks

Support us by joining the Buy Me A Coffee community and making a small donation, you can help us expand our library and ensure that music lovers everywhere can enjoy their favorite songs to the fullest. We're passionate about music, and we know you are too, so let's work together to keep the music alive.

Thank you for being a part of our community and supporting our mission to provide the best lyrics library on the internet.

Buy me a coffeeBuy us a coffee

Like this song

1 Likes

Share this song

Facebook WhatsApp Twitter Telegram LinkedIn Email

Lyrics Videos on Youtube

God Bless You, Go With God God Bless You, Go With God
Songs On Request
Listen To Our Hearts Listen To Our Hearts
Songs On Request
What A Friend We Have In Jesus What A Friend We Have In Jesus
Christ In Song Hymnal
He Gave Me A Song He Gave Me A Song
Songs On Request
Moyo Wangu Sifu Bwana Moyo Wangu Sifu Bwana
Kiswahili Praise And Worship
Amazing Grace Amazing Grace
Golden Bells