Ndikonda Kunena Ndaomboledwa
[1]
Ndikonda kunena chifukwa, Ndaomboledwa ndi mwazi!
Ndaomboledwa mwa chifundo, Ndine wace wa nthawi zonse.
CHORUS:
Ndi mwazitu (ndi mwazitu) wa Yesu, ndaomboledwa,
Ndine wace (ndine wace) kosatha, ndaomboledwa.
[2]
Ndinetu wokondwa mwa yesu, Kukondwa kosaneneka;
Ndziwa kuti kuwala kwaku Kumakhalabe ndi ine.
[3]
Ndisinkha za Mombolo wanga, Tsiku lonse ndisinkha ’Ye,
Ndiyimba wosakhala cete, Ndiyimba cikondi cace.
[4]
Ndidziwa kuti ndzamuona, Mfumu amene ndimknda;
Yemwe amanditsogolera, Ndi kundisunga usiku.
[5]
Korona ali kudikira, Mmalo anga owalawo;
Msanga ndi oyera mtimawo Ndidzakhala ndi Ambuye.
Support Mysongbooks
Support us by joining the Buy Me A Coffee community and making a small donation, you can help us expand our library and ensure that music lovers everywhere can enjoy their favorite songs to the fullest. We're passionate about music, and we know you are too, so let's work together to keep the music alive.
Thank you for being a part of our community and supporting our mission to provide the best lyrics library on the internet.