Ndidze Pafupipa
[1]
Ndidze pafupipa Mlungu wanga,
’Ngakhale ndi tsoka Mundibweza,
Koma ndiyimbabe, Mbuye m’ndikhalitse
M’fupi Ndinu.
[2]
Ngakhale ku thengo, Ndasocera,
M’mdima ndigonapo, E pa mwala.
Koma m’kulotako, Ndiyandikizanso
M’fupi Ndinu.
[3]
Pajapo ndipenya Pokwerapo,
Angelo atsika Kumwambako,
Ndo akodola Kuti ndibwerere
M’fupi ndinu
[4]
Tsono poukanso Wokondwatu,
Ndipeza pomwepo Pali Mlungu;
Ndipo masautso Andisendezanso
M’fupi Ndinu.
[5]
Podabwera Iye N’dzanka naye
Dzuwa ndu nyenyezi Zitsalira.
Pmwe ndiyimbanso, Ndidza pafupipo.
Support Mysongbooks
Support us by joining the Buy Me A Coffee community and making a small donation, you can help us expand our library and ensure that music lovers everywhere can enjoy their favorite songs to the fullest. We're passionate about music, and we know you are too, so let's work together to keep the music alive.
Thank you for being a part of our community and supporting our mission to provide the best lyrics library on the internet.