Ndidzamdziwa Mombolo Wanga
[1]
Pamene nditatha zintchito zanga zonsezo,
Nditaoloka pa tsidya la nyanja;
Cakufaci cikadzabvalatu cosafanso;
Pompo ndidzamdziwa Mombolo wanga.
CHORUS:
Ndidzamudziwa, Ndidzamudziwa, Podzaima pa mbali pacepo,
Ndidzamudziwa, ndidzamudziwa, Ndi misomali m’manja mwace.
[2]
Moyo wanga udzakondwera pakumuona,
Ndi kuona nkhope yace yowala;
Ndidzamyamika Iye ndi mtima wanga wonse,
Malo adandikonzera kumwamba.
[3]
Ee! ndidzakondwa pakuona okondedwawo
omwe ndalekana nawo m’dzikoli;
Koma n’dzamba ndaonana naye Yesuyo,
Wokondedwa wanga wopambanayo.
[4]
Kupyolera pa zipata kunka ku mzindawo,
Iye adzanditsogolera ine,
Nyimbo ya nthawi zonse ndidzayimba mokondwa;
Nditamuona Mpulumutsi wanga.
Support Mysongbooks
Support us by joining the Buy Me A Coffee community and making a small donation, you can help us expand our library and ensure that music lovers everywhere can enjoy their favorite songs to the fullest. We're passionate about music, and we know you are too, so let's work together to keep the music alive.
Thank you for being a part of our community and supporting our mission to provide the best lyrics library on the internet.