Mukhale M’mtima Mwanga
[1]
Mukhale m’mtima mwanga Ee, Yesu, Mfumuyo
Mudniyankhire ine mafunso angawo
Mukhale m’mtima mwanga, Mditsogoleretu,
Kuti ndionetsere Ukuru wanuwo.
[2]
Kacisi wa mtimanga Wayeretsedwatu,
Ulemerero wanu Uwale mkatimo;
Ndi thupi langa lonse Likhale lanulo,
Licite nthawi zonse Kufuna kwanuko
[3]
Ziwalo zanga zonse, Mzilamuliretu,
Mucite nazo zonse Kufuna kwanuko;
Ndizipereke ndense, osang’ungudzanso,
Polamulidwa nanu Mu ntchito zangazo.
[4]
Ndidzapumula ndithu Mu Mtima mwangamo,
Ndidzalindira Inu, Mukandifunatu;
Mukhale m’mtima mwanga, Ee, Yesu, Mfumuyo,
Mundiyankhire ine, Mafunso angawo.
Support Mysongbooks
Support us by joining the Buy Me A Coffee community and making a small donation, you can help us expand our library and ensure that music lovers everywhere can enjoy their favorite songs to the fullest. We're passionate about music, and we know you are too, so let's work together to keep the music alive.
Thank you for being a part of our community and supporting our mission to provide the best lyrics library on the internet.