Maziko Olimba
[1]
Maziko olimba Ambuyathuyo, Waikira inutu m’mau mwace,
Anene ciani koposa ico? Wathawira ndani kwa Mp’lumutsiyo;
Wathawira ndani kwa Mp’lumutsiyo.
[2]
Ndikati uyende mitsinjepo, Madziwo sadzakukokolola ’we;
Pakuti ndzakhala pamodzi nawe, Ndzadalitsa iwe, ndzapatule ’we;
Ndzadalitsa iwe, ndzapatula ’we.
[3]
Poyenda ’we m’moto wa mayesowo, Cisomo cangaco cikwaniradi;
Sudzapsa konsei ndangofunatu kucotsa zoipa kuyeretsa ’we,
Kucotsa zoipa kuyeretsa ’we.
[4]
Wakudza kwa Yesu kubisalako, Sindimataya kunjatu kwa mdaniyo;
Ngakhale adani amgwedezetu, Sindimsiya konse, sindimsiyatu;
Sindimsiya konse, sindimsiyatu.
Support Mysongbooks
Support us by joining the Buy Me A Coffee community and making a small donation, you can help us expand our library and ensure that music lovers everywhere can enjoy their favorite songs to the fullest. We're passionate about music, and we know you are too, so let's work together to keep the music alive.
Thank you for being a part of our community and supporting our mission to provide the best lyrics library on the internet.