Kodi Uli Kulemedwa
[1]
Kodi uli kulemedwa ndi zoipazo?
Idza kuno ati Yesu, Pumako.
[2]
Ndikamzindikira n’inji Mbuye wangayo?
Ali ndi mabala m’manja mwacemo.
[3]
Kodi ali ndi cilemba m’mphumi mwacemo?
E! Cilembaco ca minga cirimo.
[4]
Ndikampeza ndikamtsata ninji pansi?
Masauko ndi misozi ziripo.
[5]
Ndikamfunafuna Iye ndipezenjiko?
Kumariza kwa cisoni conse.
[6]
Ndikampempha anditenge ati bwanji ko?
Ati Yesu Idza msanga, idzatu.
[7]
Kukamtsata, kukampeza ndisaukanji?
Oyera, atumwi, ati idzani.
Amen.
Support Mysongbooks
Support us by joining the Buy Me A Coffee community and making a small donation, you can help us expand our library and ensure that music lovers everywhere can enjoy their favorite songs to the fullest. We're passionate about music, and we know you are too, so let's work together to keep the music alive.
Thank you for being a part of our community and supporting our mission to provide the best lyrics library on the internet.