Inde Ndifuna Kumvatu
[1]
Inde ndifuna kumvatu, Za cikondi caceco,
Ca Yesu Mbuye wangayo, Zomwe anamva kalelo.
CHORUS:
E! Zina za Yesu, E! zina za Yesu,
Inde, ndilira mmtimamo, Cipulumutso caceco.
[2]
Zina za Yesu ndimvetu Kuti ndicite zacezo
Mzimu Woyera mudzetu, Ndiphunzitseni zonsezo.
[3]
Yesu ndi mmau mwacemo, Inde ndiceza nayeyo,
Liu ndimamva mbukumo, Ndlo la Yesu Mbuyeyo.
[4]
Zina za Yesu mmwambamo, Ali pa mpando pacepo,
Udze Ufumu wacewo, Ndiyetu Mfumu ponsepo.
Support Mysongbooks
Support us by joining the Buy Me A Coffee community and making a small donation, you can help us expand our library and ensure that music lovers everywhere can enjoy their favorite songs to the fullest. We're passionate about music, and we know you are too, so let's work together to keep the music alive.
Thank you for being a part of our community and supporting our mission to provide the best lyrics library on the internet.