Dziko Ai, Koma Yesu
[1]
Dziko ai, Koma Yesu, Dziko ndi lacabetu;
Nsisi zace zikhalitsa Nthawi zonse yemweyo.
CHORUS:
Nsisi zace n’zazikuru, Ndi cikondi cacenso;
Ciombolo cozizwitsa, Moyotu wosathawo!
[2]
Dziko ai, koma Yesu, Wondisangalatsa ’ne;
Iye andiyang’anira, Nkana m’bvuto ndi’mbabe.
[3]
Dziko ai, Koma Yesu, Ndiyang’ane Iyeyo;
Pa ulendo wanga wonse, Andiunikira ’ne.
[4]
Dziko ai, Koma Yesu, Mtandawo ndigwiradi;
Mpakatu maso ndi maso, Ndidzamone Mbuyeyo.
Support Mysongbooks
Support us by joining the Buy Me A Coffee community and making a small donation, you can help us expand our library and ensure that music lovers everywhere can enjoy their favorite songs to the fullest. We're passionate about music, and we know you are too, so let's work together to keep the music alive.
Thank you for being a part of our community and supporting our mission to provide the best lyrics library on the internet.