Akristu Tiyeni
[1]
Akristu tiyeni! Nkhondo tigwira,
Yesu Mbuye wathu, Atitsogoza,
Ona mbuye yekha, Atithanziza;
Ndi mbendera yace, Tiyitsatira.
CHORUS
Akristu tiyeni! Nkhondo tigwire,
Yesu Mbuye wathu, Atitsogoza.
[2]
Nkhondo ya Satana, Msanga ithawa,
Akristu tiyeni, Tidzapambana;
Mphamvu zace zitha, Yesu titama;
Timbani anzathu Nyimbo tikweza.
[3]
Gulu larikulu, Adza Akristu;
Titsatana namwo, Ana a Mlungu;
Sitipatukana, Tonse tikhala,
ndi mtima umodzi, Timakondana.
[4]
Zonse za pa dziko, Zidzatheratu;
Koma mpingo wace, Ukhalitsabe;
Mphamvu ya Satana, idzalefuka;
Yesu nalonjeza ndidzalimbitsa.
[5]
Idzani Akristu, Kutithandiza,
Nyimbo za Mulungu, tidzayimbitsa;
Kristu ayenera, Ndiye Mfumuyo,
Tidzalemekeza, Nthawi zonsezo.
Support Mysongbooks
Support us by joining the Buy Me A Coffee community and making a small donation, you can help us expand our library and ensure that music lovers everywhere can enjoy their favorite songs to the fullest. We're passionate about music, and we know you are too, so let's work together to keep the music alive.
Thank you for being a part of our community and supporting our mission to provide the best lyrics library on the internet.